Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 7:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kucokera poturuka dzuwa, ali naco cizindikilo ca Mulungu wamoyo: ndipo anapfuula ndi mau akuru kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,

3. nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza cizindikilo akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.

4. Ndipo ndinamva ciwerengo ca iwo osindikizidwa cizindikilo, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa cizindikilo mwa mafuko onse a ana a Israyeli,

5. Mwa pfuko la Yuda anasindikizidwa cizindikilo zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri:

6. Mwa pfuko la Aseri zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Nafitali zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri:

7. Mwa pfuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Levi zikwi khumi ndiziwiri:Mwa pfuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri:

8. Mwa pfuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Benjamini anasindikizidwa cizindikilo zikwi khumi ndi ziwiri.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 7