Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 4:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo zamoyozo zinai, conse pa cokha cinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

9. Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, kwa iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,

10. akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa iye wakukhala pa mpando wacifumu, namlambira iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao ku mpando wacifumu, ndi kunena,

11. Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; cifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa cifuniro canu zinakhala, nizinalengedwa.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 4