Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 21:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwace kunafanana ndi mwala wa mtengo wace woposa, Dgati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;

12. nukhala nalo linga lalikuru ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi mama olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israyeli;

13. kum'mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwela zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu.

14. Ndipo linga la mudzi linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

15. Ndipo iye wakulankhula ridi ine anali nao muyeso, bango lagolidi, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zace, ndi linga lace.

16. Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa; utali wace ulingana ndi kupingasa kwace: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wace, ndi kupingasa kwace, ndi kutalika kwace zilingana.

17. Ndipo anayesa linga lace, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.

18. Ndipo mirimo ya linga lace ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 21