Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 19:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo mau anacokera ku mpando wacifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ace onse, akumuopa iye, ang'ono ndi akuru.

6. Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikuru, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti acita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

7. Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.

8. Ndipo anampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

9. Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10. Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.

11. Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wochedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nacita nkhondo molungama.

12. Ndipo maso ace ali lawi la moto, ndi pamutu pace pali nduwira zacifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma iye yekha.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 19