Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 18:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Cifukwa cace miliri yace idzadzam'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; cifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.

9. Ndipo mafumu a dziko ocita cigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwace, poima patali,

10. cifukwa cakuopa cizunzo cace, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, Babulo, mudzi wolimba! pakuti m'ora limodzi cafika ciweruziro canu.

11. Ndipo ocita malonda a m'dziko adzalira nadzaucitira cifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

12. malonda a golidi, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wace, ndi a ngale, ndi a nsaru yabafuta, ndi a cibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya pfungo lokoma, ndi cotengera ciri conse ca minyanga ya njobvu, ndi cotengera ciri conse camtengo wa mtengo wace wapatali, ndi camkuwa ndi cacitsulo, ndi cansangalabwi;

13. ndi kinamomo ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.

14. Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakucokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.

15. Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali cifukwa ca kuopa cizunzo cace, nadzalira, ndi kucita cifundo;

16. nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuru wobvala bafuta ndi cibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wace, ndi ngale!

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 18