Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 17:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa citsutso ca mkazi wacigololo wamkuru, wakukhala pa madzi ambiri,

2. amene mafumu a dziko anacita cigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa cigololo cace.

3. Ndipo ananditenga kumka nane kucipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pacirombo cofiiritsa, codzala ndi maina a mwano, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

4. Ndipo mkazi anabvala cibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wace, ndi ngale; nakhala naco m'dzanja lace cikho cagolidi codzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za cigololo cace,

5. ndipo pamphumi pace padalembedwa dzina, CINSINSI, BABULO WAUKURU AMAI WA ACIGOLOLO NDI WA ZONY ANSITSA ZA DZIKO.

6. Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukuru.

7. Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa cifukwa ninji? ine ndidzakuuza iwe cinsinsi ca mkazi, ndi ca cirombo cakumbereka iye, cokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

8. Cirombo cimene unaciona cinaliko, koma kulibe; ndipo cidzaturuka m'phompho, ndi kunka kucitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo ciyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona cirombo, kuti cinaliko, ndipo kulibe, ndipo cidzakhalako.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 17