Ndipo ananditenga kumka nane kucipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pacirombo cofiiritsa, codzala ndi maina a mwano, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.