Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 15:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

5. Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kacisi wa cihema ca umboni m'Mwamba:

6. Ndipo anaturuka m'Kacisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala mwala woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolidi pacifuwa pao,

7. Ndipo cimodzi ca zamoyo zinai cinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 15