Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 14:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo anawatsata mngelo wina, wacitatu, nanena ndi mau akuru, Ngati wina alambira ciromboco, ndi fane lace, nalandira lembapamphumi pace, kapena pa dzanja lace,

10. iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'cikho ca mkwiyo wace; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa j

11. ndipo utsi wa kuzunza kwao tukwera ku nthawiza nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku: iwo akulambira ciromboco ndi fano lace, ndi iye ali yense akalandira lemba la dzina lace.

12. Pano pali cipiriro ca oyera mtima, ca iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi cikhulupiriro ca Yesu.

13. Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti nchito zao zitsatana nao pamodzi.

14. Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa munthu, wakukhala naye korona wagolidi pamutu pace, ndi m'dzanja lace zenga lakuthwa.

15. Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi, wopfuulandi mau akuru kwa iye wakukhala pamtambo, Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zacetsa.

16. Ndipo iye wokhala pamtambo anaponya zenga lace padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.

17. Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi ali m'Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso.

18. Ndipo mngelo wina anaturuka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; napfuula ndi mau akuru kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, 1 Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zace zapsa ndithu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 14