Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 14:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti nchito zao zitsatana nao pamodzi.

14. Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa munthu, wakukhala naye korona wagolidi pamutu pace, ndi m'dzanja lace zenga lakuthwa.

15. Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi, wopfuulandi mau akuru kwa iye wakukhala pamtambo, Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zacetsa.

16. Ndipo iye wokhala pamtambo anaponya zenga lace padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.

17. Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi ali m'Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso.

18. Ndipo mngelo wina anaturuka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; napfuula ndi mau akuru kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, 1 Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zace zapsa ndithu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 14