Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 13:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.

8. Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,

9. N gati wina ali nalo khutu, amve.

10. N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.

11. Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.

12. Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.

13. Ndipo cicita zizindikilo zazikuru, kutinso citsitse moto ucokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.

14. Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.

15. Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.

16. Ndipo cicita kuti onse, ang'ono ndi akuru, acuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire cilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 13