Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 11:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo mngelo wacisanu ndi ciwiri anaomba, ndipo panakhala mau akulu m'Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wace: ndipo adzacita ufumu kufikira nthawi za nthawi.

16. Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yacifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu,

17. nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikuru, ndipo mwacita ufumu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 11