Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 4:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma kwa iye amene sacita, koma akhulupirira iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, cikhulupiriro cace ciwerengedwa cilungamo.

6. Monganso Davide anena za mdalitso wace wa munthu, amene Mulungu amwerengera cilungamo copanda nchito,

7. ndi kuti,Odala iwo amene akhululukidwa kusayeruzika kwao,Nakwiriridwa macimo ao,

8. Wodala munthu amene Mulungu samwerengera ucimo.

9. Mdalitso umenewu tsono uli kwa odulidwa kodi, kapena kwa osadulidwa omwe? pakuti timati, Cikhulupiriro cace cinawerengedwa kwa Abrahamu cilungamo.

10. Tsono cinawerengedwa bwanji? m'mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa;

11. ndipo iye analandira cizindikilo ca mdulidwe, ndico cosindikiza cilungamo ca cikhulupiriro, comwe iye anali naco asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti cilungamo ciwerengedwe kwa iwonso;

12. ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a cikhulupiriro cija ca kholo lathu Abrahamu, cimene iye anali naco asanadulidwe.

13. Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowanyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace mwa Lamulo, koma mwa cilungamo ca cikhulupiriro.

14. Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo cikhulupiriro eayesedwa cabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pace;

15. pakuti cilamulo cicitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa.

Werengani mutu wathunthu Aroma 4