Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 1:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.

5. Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iri yonse,Iwe ndiwe Mwana wanga,Lero ine ndakubala Iwe?ndiponso,Ine ndidzakhala kwa iye Atate,Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana?

6. Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire iye angelo onse a Mulungu.

7. Ndipo za angelo anenadi,Amene ayesa angelo ace mizimu,Ndi omtumikira iye akhale lawi lamoto;

8. Koma ponena za Mwana, ati,Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi;Ndipo ndodo yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

9. Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa;Mwa ici Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozaniNdi mafuta a cikondwerero ceni ceni koposa anzanu.

10. Ndipo,Inu, Ambuye, paciyambipo munaika maziko ace a dziko,Ndipo miyamba iri nchito ya manja anu;

11. Iyo idzatayika; komatu mukhalitsa;Ndipo iyo yonse idzasuka mongamaraya;

12. Ndi monga copfunda mudzaipindaMonga maraya, ndipo idzasanduka;Koma Inu ndinu yemweyo,Ndipo zaka zanu sizidzatha.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 1