Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. KALE Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyana-siyana,

2. koma pakutha pace pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;

3. ameneyo, pokhala ali cinyezimiro ca ulemerero wace, ndi cizindikilo ceni ceni ca cikhalidwe cace, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yace, m'mene adacita ciyeretso ca zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,

4. atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.

5. Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iri yonse,Iwe ndiwe Mwana wanga,Lero ine ndakubala Iwe?ndiponso,Ine ndidzakhala kwa iye Atate,Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana?

6. Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire iye angelo onse a Mulungu.

7. Ndipo za angelo anenadi,Amene ayesa angelo ace mizimu,Ndi omtumikira iye akhale lawi lamoto;

8. Koma ponena za Mwana, ati,Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi;Ndipo ndodo yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

9. Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa;Mwa ici Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozaniNdi mafuta a cikondwerero ceni ceni koposa anzanu.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 1