Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 3:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taonani, cikondico Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere. Mwa ici dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira iye.

2. Okondedwa, tsopano riri ana a Mulungu, ndipo sicinaoneke cimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka iye, tidzakhala ofanana ndi iye, Pakuti tidzamuona iye monga ali.

3. Ndipo yense wakukhala naco ciyembekezo ici pa iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.

4. Yense wakucita cimo acitanso kusayeruzika; ndipo cimo ndilo kusayeruzika.

5. Ndipo mudziwa kuti iyeyu anaonekera kudzacotsa macimo; ndipo mwa Iye mulibe cimo.

6. Yense wakukhala mwa iye sacimwa; yense wakucimwa sanamuona iye, ndipo sanamdziwa iye.

7. Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakucita colungama af wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:

8. iye wocita cimo ali wocokera mwa mdierekezi, cifukwa mdierekezi amacimwa kuyambira paciyambi. Kukacita ici Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge nchito za mdierekezi,

9. Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu.

10. M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosacita cilungamo siali wocokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wace.

11. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace:

12. osati monga Kaini anali wocokera mwa woipayo, namupha mbale wace. Ndipo anamupha iye cifukwa ninji? Popeza nchiro zace zinali zoipa, ndi za mbaie wace zolungama.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 3