Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 1:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu: Cisomo kwa inu ndi mtendere.

2. Tiyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu nonse, ndi kukumbukila inu m'mapemphero athu;

3. ndi kukumbukila kosalekeza nchito yanu ya cikhulupiriro, ndi cikondi cocitacita, ndi cipiriro ca ciyembekezo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;

4. podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, cisankhidwe canu,

5. kuti Vthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kucuruka kwakukuru; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu cifukwa ca inu.

6. Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'cisautso cambiri, ndi cimwemwe ca Mzimu Woyera;

7. kotero kuti munayamba kukhala inu citsanzo kwa onse akukhulupira m'Makedoniya ndi m'Akaya.

8. Pakuti kuturuka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Makedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse cikhulupiriro canu ca kwa Mulungu cidaturuka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.

9. Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembeoukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weni weni wamoyo,

10. ndi kulindirira Mwana wace acokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulinkudza.

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 1