Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 8:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakuturuka, kapena wakulowa, cifukwa ca wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzace.

11. Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu.

12. Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zace, ndi nthaka idzapatsa zobala zace, ndi miyamba Idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, cikhale colowa cao.

13. Ndipo kudzacitika kuti, monga munali cotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israyeli, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala codalitsa naco; musaope, alimbike manja anu.

14. Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndil nalingirira kucitira inu coipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka;

15. momwemonso ndinalingirira masiku ano kucitira cokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 8