4. Aneneri ace ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza cilamulo.
5. Yehova pakati pace ali wolungama; sadzacita cosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera ciweruzo cace poyera, cosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.
6. Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungondya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.
7. Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pace pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, nabvunditsa macitidwe ao onse.
8. Cifukwa cace, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.
9. Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.