Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zefaniya 3:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mudzi wozunza!

2. Sanamvera mau, sanalola kulangizidwa; sanakhulupirira Yehova, sanayandikira kwa Mulungu wace.

3. Akalonga ace m'kati mwace ndiwo mikango yobangula; oweruza ace ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.

4. Aneneri ace ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza cilamulo.

5. Yehova pakati pace ali wolungama; sadzacita cosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera ciweruzo cace poyera, cosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.

6. Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungondya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.

7. Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pace pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, nabvunditsa macitidwe ao onse.

8. Cifukwa cace, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.

9. Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.

Werengani mutu wathunthu Zefaniya 3