Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 8:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ace ndi mudzi wace ndi dziko lace;

2. ndipo uzimcitira Ai ndi mfumu yace monga umo unamcitira Yeriko ndi mfumu yace; koma zofunkha zace ndi ng'ombe zace mudzifunkhire nokha; udziikire anthu aja lire kukhonde kwa mudzi.

3. Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

4. nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse;

5. ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mudzi; ndipo kudzali, pamene aturuka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao;

6. ndipo adzaturuka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mudzi; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba pala; nafenso tidzathawa pamaso pao;

7. pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mudzi; pakuti Yehova Mulungu wanu adzaupereka m'manja mwanu.

8. Ndipo kudzali, mutagwira mudzi, muzitentha mudziwo ndi moto; muzicita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

9. Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

10. Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akuru a Israyeli, pamaso pa anthu a ku Ai.

11. Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mudzi, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali cigwa.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 8