Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 7:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Koma m'mawa adzakuyandikitsani, pfuko ndi pfuko; ndipo kudzali kuti pfukoli Yehova aliulula lidzayandikira mwa zibale zace; ndi cibale Yehova aciulula cidzayandikira monga mwa a nyumba ace; ndi a m'nyumbawo Yehova awaulula adzayandikira mmodzi mmodzi.

15. Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali naco coperekedwaco adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo cifukwa analakwira cipangano ca Yehova, ndi cifukwa anacita copusa m'Israyeli.

16. Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israyeli, pfuko ndi pfuko; ndi pfuko la Yuda linagwidwa;

17. nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira cibale ca Azari; nayandikizitsa cibale ca Azari, mmodzi mmodzi, nagwidwa Zabidi;

18. nayandikizitsa a m'nyumba yace mmodzi mmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimu, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda anagwidwa.

19. Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, ucitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze iye; nundiuze tsopano, wacitanji? usandibisire.

20. Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndacimwira Yehova Mulungu wa Israyeli, ndacita zakuti zakuti;

21. pamene ndinaona pazofunkha maraya abwino a ku Babulo, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi cikute cagolidi, kulemera kwace masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pacepo.

22. Pamenepo Yoswa anatuma mithenga, iwo nathamangira kuhema; ndipo taonani, zidabisika m'hema mwace ndi siliva pansi pace.

23. Ndipo anazicotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israyeli, nazitula pamaso pa Yehova.

24. Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi marayawo, ndi cikute cagolidi, ndi ana ace amuna ndi akazi, ndi ng'ombe zace, ndi aburu ace, ndi nkhosa zace, ndi hema wace ndi zace zonse; nakwera nazo ku cigwa ca Akori.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 7