Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 6:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa cifukwa ca ana a Israyeli, panalibe woturuka, panalibenso wolowa.

2. Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yace, ndi ngwazi zace.

3. Ndipo muzizungulira mudzi Inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.

4. Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga: za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muzizungulira mudziwo kasanu ndi kawirio ndi ansembe aziliza mphalasazo.

5. Ndipo kudzakhala kuti akaliza cilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse apfuule mpfuu yaikuru; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwace.

6. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la cipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.

7. Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mudzi, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.

8. Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la cipangano ca Yehova linawatsata.

9. Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m'mbuyo anatsata likasa, ansembe ali ciombere poyenda iwo.

10. Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamapfuula, kapena kumveketsa mau anu, asaturuke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Pfuulani; pamenepo muzipfuula.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 6