Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 5:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordano, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku Nyanja ya Mcere anamvakuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordano pamaso pa ana a Israyeli mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo cifukwa ca ana a Israyeli.

2. Nthawi imeneyo Yehova anati kwa Yoswa, Udzisemere mipeni yamiyala, nudulenso ana a Israyeli kaciwiri.

3. Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israyeli pa Gibeya Naraloti.

4. Koma cifukwa cakuti Yoswa anawadula ndi ici: anthu onse oturuka m'Aigupto, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'cipululu panjira, ataturuka m'Aigupto.

5. Pakuti anthu onse anaturukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'cipululu panjira poturuka m'Aigupto sanadulidwa.

6. Pakuti ana a Israyeli anayenda m'cipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo oturuka m'Aigupto udatha, cifukwa ca kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci.

7. Koma ana ao amuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadula panjira.

8. Ndipo kunali, atatha kudula mtundu wonse, anakhala m'malo mwao m'cigono mpaka adacira.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 5