Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 24:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mapfuko onse a Israyeli ku Sekemu, naitana akulu akulu a Israyeli ndi akuru ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzilangiza pamaso pa Mulungu.

2. Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu yina iwowa.

3. Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kucurukitsa mbeu zace ndi kumpatsa Isake,

4. Ndi kwa Isake ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lace lace; koma Yakobo ndi ana ace anatsikira kumka ku Aigupto.

5. Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aigupto, monga ndinacita pakati pace; ndipo nditatero ndinakuturutsani.

6. Ndipo ndinaturutsa atate anu m'Aigupto; ndipo munadzakunyanja; koma Aaigupto analondola atate anu ndi magareta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.

7. Ndipo pamene anapfuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aaigupto nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya cocita Ine m'Aigupto; ndipo munakhala m'cipululu masiku ambiri.

8. Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordano; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanu lanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.

9. Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Moabu, anauka naponyana ndi Israyeli; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;

Werengani mutu wathunthu Yoswa 24