Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 18:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati pa dziko, ndi kulilemba, oimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pane pamaso pa Yehova pa Silo.

9. Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yace, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku cigono ku Silo.

10. Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israyeli dziko, monga mwa magawo ao.

11. Ndipo maere a ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anaturuka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.

12. Ndipo malire ao a kumpoto anacokera ku Yordano; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi maturukiro ace anali ku cipululu ca Beti-aveni.

13. Ndipo malire anapitirirapo kumka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Beteli, kumwela; ndi malire anatsikira kumka ku Atarotu-adara, ku phiri lokhala kumwela kwa Betihoroni wa kunsi.

14. Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kumka kumwela, kucokera ku phiri pokhala patsogolo pa Beti-horoni, kumwela kwace; ndi maturukiro ace anali ku Kiriyatibaala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.

15. Ndipo mbali ya kumwela inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; naturuka malire kumka kumadzulo, naturuka kumka ku citsime ca madzi a Nefitoa;

16. natsikira malire kumka polekezera phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca mwana wa Hinomu, ndico ca m'cigwa ca Refai kumpoto; natsikira ku cigwa ca Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwela, natsikira ku Enirogeli;

Werengani mutu wathunthu Yoswa 18