Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 17:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. kumwera nkwa Efraimu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ace ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Aseri, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara.

11. Ndipo m'Isakara ndi m'Aseri Manase anali nao Betiseani ndi midzi yace, ndi Ibleamu ndi midzi yace, ndi nzika za Doro ndi midzi yace, ndi nzika za Eni-doro ndi midzi yace, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yace, ndi nzika za Megido ndi midzi yace; dziko la mapiri atatu.

12. Koma ana a Manase sanatha kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akananjanafuna kukhala m'dziko lija.

13. Ndipo kunali pamene ana a lsrayeli atakula mphamvu anasonkhetsa Akanani osawaingitsa onse.

14. Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji colowa cathu camaere cimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?

15. Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefai; akakuceperani malo ku phiri la Efraimu.

16. Ndipo ana a Yosefe anati, Kuphiriko sikudzatifikira; ndipo Akananionse akukhala m'dziko la cigwa ali nao magareta acitsulo, iwo akukhala m'Bete-Seani, ndi midzi yace ndi iwo omwe akukhala m'cigwa ca Yezereli.

17. Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m'nyumba ya Yosefe, kwa Efraimu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikuru; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha;

18. koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi maturukiro ace adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magareta acitsulo, angakhale ali amphamvu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 17