Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 16:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo gawo La ana a Yosefe linaturuka kucokera ku Yordano ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum'mawa, kucipululu, nakwera kucokera ku Yeriko kumka kumapiri ku Beteli;

2. naturuka ku Beteli kumka ku Luzi, napitirira kumka ku malire a Aariki, ku Atarotu;

3. natsikira kumadzulo kumka ku malire a Ayafeleti, ku malire a Beti-horoni wa kunsi, ndi ku Gezeri; ndi maturukiro ace anali kunyanja.

4. Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efraimu analandira colowa cao,

5. Ndipo malire a ana a Efraimu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a colowa cao kum'mawa ndiwo Atarotu-Adara, mpaka Betihoroni wa kumtunda;

6. naturuka malire kumadzulo ku Mikametatu kumpoto; nazungulira malire kum'mawa kumka ku Taanatu-silo, naupitirira kum'mawa kwace kwa Yanoa:

7. natsika kucokera ku Yanoa, kumka ku Atarotu, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, naturuka ku Yordano.

8. Kuyambira ku Tapua malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi maturukiro ace anali kunyanja. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Efraimu monga mwa mabanja ao;

Werengani mutu wathunthu Yoswa 16