16. Malire ao anayambira ku Aroeri wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa cigwa ndi cidikha conse ca ku Medeba;
17. Hesiboni ndi midzi yace yonse yokhala pacidikha; Diboni, ndi Bamoto-baala ndi Betibaala-Meoni;
18. ndi Yahaza ndi Kedemotu, ndi Mefaata;
19. ndi Kinyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kucigwa;
20. ndi Beti-peori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beti-yesimotu;
21. ndi midzi yonse ya kucidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wocita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko.
22. Ana a Israyeli anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.
23. Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordano ndi malire ace. Ndico colandira ca ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.
24. Ndipo Mose anapatsira pfuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao.
25. Ndipo malire ao ndiwo Yazeri, ndi midzi yonse ya Gileadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroeri, wokhala cakuno ca Raba;
26. ndi kuyambira Hesiboni mpaka Ramati-Mizipe, ndi Betonimu; ndi kuyambira Mahanaimu mpaka malire a Dibiri;
27. ndipo m'cigwa Betiharamu, ndi Beti-nimra, ndi Sukoti, ndi Zafoni, cotsala ca ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yoidano ndi malire ace, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordano kum'mawa.
28. Ici ndi colowa ca ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.