Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 13:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma ana a Israyeli sanainga Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israyeli, mpaka lero lino.

14. Koma pfuko la Levi sanalipatsa colowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israyeli, zocitika ndi moto, ndizo colowa cace, monga iye adanena naye.

15. Ndipo Mose anapatsira pfuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao.

16. Malire ao anayambira ku Aroeri wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa cigwa ndi cidikha conse ca ku Medeba;

17. Hesiboni ndi midzi yace yonse yokhala pacidikha; Diboni, ndi Bamoto-baala ndi Betibaala-Meoni;

18. ndi Yahaza ndi Kedemotu, ndi Mefaata;

19. ndi Kinyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kucigwa;

20. ndi Beti-peori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beti-yesimotu;

21. ndi midzi yonse ya kucidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wocita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko.

22. Ana a Israyeli anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.

23. Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordano ndi malire ace. Ndico colandira ca ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.

24. Ndipo Mose anapatsira pfuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao.

25. Ndipo malire ao ndiwo Yazeri, ndi midzi yonse ya Gileadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroeri, wokhala cakuno ca Raba;

Werengani mutu wathunthu Yoswa 13