Koma pfuko la Levi sanalipatsa colowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israyeli, zocitika ndi moto, ndizo colowa cace, monga iye adanena naye.