Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 4:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima cifukwa ca msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

10. Ndipo Yehova anati, Unacitira cifundo msatsiwo umene sunagwirapo nchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

11. ndipo sindiyenera Ine kodi kucitira cifundo Nineve mudzi waukuru uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

Werengani mutu wathunthu Yona 4