Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 8:3-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uche dzina lace, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.

4. Cifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakupfuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, cuma ca Damasiko ndi cofunkha ca Samariya cidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asuri.

5. Ndipo Yehova ananena kwa ine kaciwirinso, nati,

6. Popeza anthu awa akana madzi a Silowa, amene ayenda pang'ono pang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;

7. cifukwa cace, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a Nyanja, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asuri ndi ulemerero wace wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zace zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.

8. Ndipo iye adzapitapitakulowa m'Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ace, kudzakwanira dziko lanu m'citando mwace, inu Imanueli.

9. Citani phokoso, anthu inu, koma mudzatyokatyoka; cherani khutu, inu nonse a maiko akutari; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka.

10. Panganani upo, koma udzakhala cabe; nenani mau, koma sadzacitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.

11. Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m'njira ya anthu awa, nati,

12. Musacinene, Ciwembu; ciri conse cimene anthu awa adzacinena, Ciwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musacite mantha.

13. Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akucititseni mantha Iye.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 8