Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 7:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israyeli, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupamnana.

2. Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efraimu. Ndipo mtima wace unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ace, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.

3. Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Turuka tsopano kukacingamira Ahazi, iwe ndi Seariyasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamariziro a mcerenje wa thamanda la pamtunda, ku khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru;

4. nukati kwa iye, Cenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, cifukwa ca zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, cifukwa ca mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.

5. Cifukwa Aramu ndi Efraimu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukucitira zoipa, nati,

6. Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timbvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pace, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeeli;

7. atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzacitidwa.

8. Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efraimu adzatyokatyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;

9. ndipo mutu wa Efraimu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.

10. Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati,

11. Udzipemphere wekha cizindikilo ca kwa Yehova Mulungu wako; pempha cam'mwakuya, kapena cam'mwamba.

12. Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova.

13. Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?

14. Cifukwa cace Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu cizindikilo; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamucha dzina lace Imanueli.

15. Iye adzadya mafuta ndi uci, pamene adziwa kukana coipa ndi kusankha cabwino.

16. Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana coipa ndi kusankha cabwino, dziko limene mafumu ace awiri udana nao lidzasyidwa.

17. Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efraimu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asuri.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 7