Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 65:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;

5. amene ati, Ima pa wekha, usadze cifupi ndi ine, pakuti ine ndiri woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.

6. Taonani, calembedwa pamaso panga; sindidzakhala cete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa cifuwa cao,

7. zoipa zanu zanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandicitira mwano pazitunda; cifukwa cace Ine ndidzayesa nchito yao yakale ilowe pa cifuwa cao.

8. Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, momwemo ndidzacita cifukwa ca atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.

9. Ndipo ndidzaturutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira colowa cao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko.

10. Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi cigwa ca Akori cidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.

11. Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mlungu wamwai gome, ndi kudzazira mlungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza;

12. ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene Ine sindinakondwera naco.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 65