Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 63:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.

6. Ndipo ndinapondereza anthu m'kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao.

7. Ndidzachula za cifundo cace ca Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wace waukuru kwa banja la Israyeli, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa cifundo cace, ndi monga mwa nchito zocuruka za cikondi cace.

8. Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangacite monyenga; comweco Iye anali Mpulumutsi wao.

9. M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pace anawapulumutsa; m'kukonda kwace ndi m'cisoni cace Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.

10. Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa cisoni mzimu wace woyera, cifukwa cace Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.

11. Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ace, nati, Ali kuti Iye amene anawaturutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lace? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wace woyera pakati pao,

12. amene anayendetsa mkono wace waulemerero pa dzanja lamanja la Mose? amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?

13. amene anawatsogolera kupitira mwa kuya monga kavalo m'cipululu osapunthwa iwo?

14. Monga ng'ombe zotsikira kucigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; comweco inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.

15. Tayang'anani kunsi, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, cangu canu ndi nchito zanu zamphamvu ziri kuti? mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi cisoni canu.

16. Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israyeli satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wacikhalire ndi dzina lanu.

17. Yehova bwanji mwatisoceretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, cifukwa ca atumiki anu, mafuko a colowa canu.

18. Anthu anu opatulika anakhala naco kanthawi kokha; adani athu apondereza kacisi wanu wopatulika.

19. Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulira konse, ngati iwo amene sanachedwa dzina lanu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 63