Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 55:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. woipa asiye njira yace, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ace, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamcitira cifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.

8. Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati Yehova.

9. Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitari kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

10. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kucokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzyala, ndi cakudya kwa wakudya;

11. momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.

12. Pakuti inu mudzaturuka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzayimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.

13. M'malo mwa mithethe mudzaturuka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamcisu; ndipo cidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati cizindikiro cosatha, cimene sicidzalikhidwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 55