M'malo mwa mithethe mudzaturuka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamcisu; ndipo cidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati cizindikiro cosatha, cimene sicidzalikhidwa.