Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 55:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kucokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzyala, ndi cakudya kwa wakudya;

11. momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.

12. Pakuti inu mudzaturuka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzayimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.

13. M'malo mwa mithethe mudzaturuka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamcisu; ndipo cidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati cizindikiro cosatha, cimene sicidzalikhidwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 55