Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 53:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wabvumbulukira yani?

2. Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pace ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.

3. Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza.

4. Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuvesa wokhomedwa wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa.

5. Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.

6. Tonse tasocera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

7. Iye anatsenderezedwa koma anadzicepetsa yekha osatsegula pakamwa pace; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pace.

8. Anacotsedwa ku cipsinjo ndi ciweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wace? pakuti walikhidwa kunja kuno; cifukwa ca kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.

9. Ndipo anaika manda ace pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yace, ngakhale Iye sanacita ciwawa, ndipo m'kamwa mwace munalibe cinyengo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 53