Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 50:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atero Yehova, Kalata wa cilekaniro ca amako ali kuti amene ndinamsudzula naye? pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona cifukwa ca zoipa zanu munagulitsidwa, ndi cifukwa ca kulakwa kwanu amanu anacotsedwa.

2. Cifukwa canji ndinafika osapeza munthu? ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja yaikuru, ndi kusandutsa mitsinje cipululu; nsomba zace zinunkha cifukwa mulibe madzi, nizifa ndi ludzu.

3. Ndibveka thambo ndi kuda, ndi kuyesa ciguduli copfunda cace.

4. Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akucirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi im'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.

5. Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.

6. Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulabvulidwa.

7. Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; cifukwa cace sindinasokonezedwa; cifukwa cace ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 50