Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 47:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Cifukwa cace tsono, imva ici, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;

9. koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa unyinji wa matsenga ako, ndi pakati pa maphenda ako ambirimbiri.

10. Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi cidziwitso cako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.

11. Cifukwa cace coipa cidzafika pa iwe; sudzadziwa kuca kwace, ndipo cionongeko cidzakugwera; sudzatha kucikankhira kumbali; ndipo cipasuko cosacidziwa iwe cidzakugwera mwadzidzidzi.

12. Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira nchito ciyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

13. Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.

14. Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha ku mphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.

15. Zinthu zomwe unagwira nchito yace, zidzatero nawe; iwo amene anacita malonda ndi iwe ciyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwace; sipadzakhala wopulumutsa iwe.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 47