Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 45:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwacabe; Ine Yehova ndinena cilungamo, ndinena zimene ziri zoona.

20. Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani cifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mlungu wosakhoza kupulumutsa.

21. Nenani inu, turutsani mlandu wanu; inde, acite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ici ciyambire nthawi yakale? ndani wanena ici kale? kodi si ndine Yehova? ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.

22. Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.

23. Ndadzilumbira ndekha, mau acokera m'kamwa mwanga m'cilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.

24. Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli cilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 45