16. Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu;
17. amene aturutsa gareta ndi ka valo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.
18. Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale.
19. Taonani, ine ndidzacita cinthu catsopano; tsopano cidzaoneka; kodi simudzacidziwa? Ndidzakonzadi njira m'cipululu, ndi mitsinje m'zidalala.
20. Nyama za m'thengo zidzandilemekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; cifukwa ndipatsa madzi m'cipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;
21. anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.
22. Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israyeli.
23. Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi zonunkhira.
24. Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndarama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi macimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.