Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 43:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.

12. Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wacilendo pakati pa inu; cifukwa cace inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.

13. Inde ciyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira nchito, ndipo ndani adzaletsa?

14. Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israyeli: Cifukwa ca inu ndatumiza ku Babulo, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Akasidi m'ngalawa za kukondwa kwao.

15. Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israyeli, Mfumu yanu,

16. Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu;

17. amene aturutsa gareta ndi ka valo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.

18. Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale.

19. Taonani, ine ndidzacita cinthu catsopano; tsopano cidzaoneka; kodi simudzacidziwa? Ndidzakonzadi njira m'cipululu, ndi mitsinje m'zidalala.

20. Nyama za m'thengo zidzandilemekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; cifukwa ndipatsa madzi m'cipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;

21. anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 43