Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 42:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzaturutsira amitundu ciweruziro.

2. Iye sadzapfuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mau ace m'khwalala.

3. Bango lophwanyika sadzalityola, ndi lawi lozirala sadzalizima; adzaturutsa ciweruzo m'zoona.

4. Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa ciweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira cilamulo cace.

5. Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi cimene cituruka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;

6. Ine Yehova ndakuitana Iwe m'cilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;

7. kuti utsegule maso akhungu, uturutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, aturuke m'nyumba ya kaidi.

8. Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.

9. Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizichula; zisanabuke ndidzakumvetsani.

10. Yimbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ace kucokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse ziri m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.

11. Cipululu ndi midzi yace ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela ayimbe, akuwe kucokera pamwamba pa mapiri.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 42