Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 41:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Khalani cete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni, tiyandikire pamodzi kuciweruziro.

2. Ndani anautsa wina wocokera kum'mawa, amene amuitana m'cilungamo, afike pa phazi lace? Iye apereka amitundu patsogolo pace, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga pfumbi ku lupanga lace, monga ciputu couluzidwa ku uta wace.

3. Iye awathamangitsa, napitirira mwamtendere; pa njira imene asanapitemo ndi mapazi ace.

4. Ndani wacipanga, nacimariza ico, kuchula mibadwo ciyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pacimariziro ndine ndemwe.

5. Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.

6. Iwo anathangata yense mnansi wace, ndi yense anati kwa mbale wace, Khala wolimba mtima.

7. Cotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golidi, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi nthobvu, Kuti kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.

8. Koma iwe, Israyeli, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 41