Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 37:4-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asuri mbuyace inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; cifukwa cace, kweza pemphero lako cifukwa ca otsala osiyidwa.

5. Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya.

6. Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilalatira Ine.

7. Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.

8. Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asuri irikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inacoka ku Lakisi.

9. Ndipo anamva anthu alinkunena za Tiraka, mfumu ya Kusi, Iye waturuka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti,

10. Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.

11. Taona, iwe wamva cimene mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?

12. Kodi milungu ya amitundu yaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefi ndi ana a Edeni amene anali m'Telasara.

13. Iri kuti mfumu ya ku Hamati, ndi mfumu ya ku Aripadi, ndi mfumu yamudzi wa ku Sefaravaimu, ya ku Hena, ndi Iveva?

14. Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m'manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15. Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova, nati,

16. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

17. Cherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Sanakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.

18. Zoonadi, Yehova, mafumu a Asuri anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.

19. Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma nchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; cifukwa cace iwo anaiononga,

20. Cifukwa cace, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwace, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.

21. Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Popeza wandipemphera za Sanakeribu mfumu ya Asuri,

22. awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi ciphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wace pambuyo pako.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 37