Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asuri mbuyace inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; cifukwa cace, kweza pemphero lako cifukwa ca otsala osiyidwa.