Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 36:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Cifukwa cace upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asuri, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.

9. Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng'ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Aigupto, kuti adzakupatsa magareta ndi apakavalo?

10. Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.

11. Ndipo Eliakimu, ndi Sebina, ndi Yoaki, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'cinenero ca Aramu; pakuti ife ticimva; ndipo musanene kwa ife m'Ciyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.

12. Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? kodi iye sananditumiza ine kwa amuna okhala palinga, kuti adye ndowe zao zao, ndi kumwa madzi ao ao ndi inu?

13. Pamenepo kazembeyo anaima, napfuula ndi mau akuru m'Ciyuda, nati, Imvani, inu, mau a mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri.

14. Mfumu itere, Musaleke Hezekiya anyenge inu; pakuti iye sadzathai kukupulumutsani:

15. ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mudzi uwu sudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.

16. Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asuri itere, Mupangane nane, turukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zace, ndi nkhuyu zace, namwe yense madzi a pa citsime cace;

17. kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu ku dziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la cakudya ndi minda yamphesa.

18. Cenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iri yonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asuri?

19. Iri kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu? kodi inapulumutsa Samariya m'manja mwanga?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 36